Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 9
Paphata pa Chichewa
Amubatha: Amugwira.
Chitsanzo: Anamubatha ali ndi mkazi wamwini.
Amudomola: Amuchotsa.
Chitsanzo: Achimwene anuwa awadomola m’gulu
lobwereketsa ngongole lija.
Amukhumula: Anamubera, kumupusitsa.
Chitsanzo: Madobadoba ena a m’tauni anamukhumula
ndalama zake.
Amukwangwanula: Kubera munthu.
Chitsanzo: Amukwangwanula ndalama zonse.
Amunamuna ogona chitseko chosatseka: Mwamuna
weniweni, wamphamvu.
Chitsanzo: Kumalola anthu ngati ife, amunamuna ogona
chitseko chosatseka.
Amuomba: Amubera. Tanthauzo lake lenileni ndi
kugunda.
Chitsanzo: Akuba amuomba ndalama zonse.
Amupatsa phuli/phuga: Chichewa cha achinyamata
chomwe chimatanthauza kuti amupatsa mimba.
Chitsanzo: Mtsikana uja wapatsidwa phuli/phuga ndi
aphunzitsi ake.
Amupyera: Mawu achipongwe onena za munthu amene
wagwidwa.
Chitsanzo: Anamupyera akuba matimati m’munda wa
agogo.
Amwandionerapati: Anthu afupiafupi.
Chitsanzo: Kodi unawaonapo Amwandionerapati?
8