Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 7
Paphata pa Chichewa
Alibe 2 koloko: Wosachedwa kupsa mtima, munthu
wovuta.
Chitsanzo: Akazi awo alibe 2 koloko. Akhoza
kukulalatirani ngati mutawaputa.
Alibe khalidwe: Ali ndi khalidwe loipa. Angatanthauzenso
munthu wopanda pabwino.
Chitsanzo: Mwanayu alibe khalidwe.
Alibe mnzake: Alibe munthu wopikisana naye.
Chitsanzo: Mtsikanayu alibe mnzake pankhani yovina.
Alibe nazo gashe: Alibe nazo ntchito.
Chitsanzo: Zoti anthu akumunena, alibe nazo gashe. Bola
zake zikuyenda.
Alibe pabwino: Alibe pokomera, samathokoza.
Chitsanzo: Munthu ameneyu alibe pabwino, ngakhale
utamuthandiza bwanji sayamika.
Alibe pogwira: Ali m’mavuto.
Chitsanzo: Gogowa alibe pogwira, ana awo onse anatsikira
kulichete.
Alibiretu ngakhale 1 tambala: Alibe kalikonse, alibiretu
ndalama.
Chitsanzo: Amandiuza kuti alibiretu ngakhale 1 tambala.
Koma titangosiyana, ndinawaona akugula tchipisi.
Alungalunga: Opanda chilema.
Chitsanzo: Wolumala uja anakwatiwa ndi munthu
walungalunga.
Amadya napondapo: Amaipitsa pamalo omwe wakhala.
Chitsanzo: Mkamwiniyu amakhala ngati wabwino pamaso
pa anthu, koma amadya napondapo.
6