Paphata pa Chichewa
Ali mafupa okhaokha: Waonda kwambiri.
Chitsanzo: Malume anu angotsala mafupa okhaokha.
Ali mutu gwa: Mawuwa amanenedwa monyoza kwa
munthu wosamva.
Chitsanzo: Tamuoneni, ali mutu gwa ngati sakumva!
Ali ndi mano achipani: Ali ndi mano achikasu, ali ndi
chiseyeye. Mawu amenewa anayamba chifukwa cha
mtundu womwe chipani cha UDF chinkagwiritsa ntchito.
Ndiye ponena monyoza za munthu yemwe mano ake ndi
achikasu, ankangoti ali ndi mano achipani.
Chitsanzo: Atangomwetulira mpamene ndinadziwa kuti ali
ndi mano achipani.
Ali ndi mfundo: Amayankhula zomveka, amanena
zanzeru.
Chitsanzo: Mwanayu ali ndi mfundo.
Ali ndi mtima: Amene akundifunabe, amene
wandikonda.
Chitsanzo: Amene ali ndi mtima anditsate.
Ali ndi mwana agwiritse: Zafika povuta, mpofunika
kuchita khama, kulimba nazo.
Chitsanzo: Zafikapa, ali ndi mwana agwiritse!
Ali ndi thupi: Ndi wonenepa.
Chitsanzo: Akazi awo ali ndi thupi.
Ali ndi ziwindi: Ndi wamakani.
Chitsanzo: Mwanayu ali ndi ziwindi.
Ali pabwino: Zinthu zikuwayendera.
Chitsanzo: Anzathuwa ali pabwino, zawo zikuwayendera.
5