Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 5
Paphata pa Chichewa
Akuka: Apongozi.
Chitsanzo: Kunyumba kwabwera akuka anga.
Akukupondererani: Akukuposani.
Chitsanzo: Mwanayutu akukupondererani m’kalasi muno.
Akuluakulu n’kudzala: Akuluakulu ndi amene amathetsa
nkhani. Nkhani iliyonse imakathera kwa iwowo.
Chitsanzo: Tabwera kwa inu chifukwa tikudziwa kuti
akuluakulu n’kudzala.
Akunjira: Alendo.
Chitsanzo: Akunjira, takulandirani!
Akupeza bwino: Achira.
Chitsanzo: Amadwala aja tsopano akupeza bwino.
Akusowa pogwira: Akuvutika kwambiri.
Chitsanzo: Amene sanakolole chaka chatha akusowa
pogwira.
Ali chabe: Alibe kanthu, ali chimanjamanja.
Chitsanzo: Angobwerako ali chabe.
Ali m’dothi: Kugwa kwambiri (kuphofomoka)
Chitsanzo: Mnzakeyo anachipulumutsa chibakera, ndipo
ndinangoona ali m’dothi.
Ali m’madzi: Ali m’mavuto, akumana nazo.
Chitsanzo: Akangomugwira ali m’madzi.
Ali m’maso:
(a) Asanagone.
Chitsanzo: Mukamadzabwera mudzandipeza ndili m’maso.
(b) Asanamwalire.
Chitsanzo: Mukanabwera dzulo mukanawapeza ali
m’maso. Atisiya m’mawa womwewu.
4