Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 4
Paphata pa Chichewa
Adawatulukira:
(a) Adawachezera
Chitsanzo: Atabwera kuno anapita kukawatulukira agogo.
(b) Anazindikira chinyengo chawo.
Chitsanzo: Adawatulukira kuti amanena bodza.
Adzukulu: Anthu okumba manda komanso kuika maliro,
mawuwa amatanthauzanso ana a mwana wako.
Chitsanzo: Adzukuluwo anagwira wanjinga
n’kumumangirira pamtengo pofuna kumupatsa phunziro
kuti asadzadutsenso pamanda atakwera njinga.
Agwireni ntchito: Amenyeni.
Chitsanzo: Anyamata aja ndi amenewa, agwireni ntchito.
Akadayenda: Ali ndi pakati koma sanachirebe.
Chitsanzo: “Kodi ali ndi mwana tsopano?” “Ayi
akadayenda.”
Akalimbalimba: Akachita makani.
Chitsanzo: Akakalimbalimba mukangomumanga.
Akamwiniatsatana: Kagulu ka nyenyezi zisanu zowala
bwino.
Chitsanzo: Wawaona akamwiniatsatana?
Akapamba okhala pachifu: Anthu osauka kwambiri,
osowa pokhala.
Chitsanzo: Ife ndiye ndi akapamba okhala pachifu,
angatiwerengere ife!
Akucheperakaba: Ndi mwana.
Chitsanzo: Amene uja akucheperakaba, sangandimenye.
Akuchita nseru: Akufuna kusanza.
Chitsanzo: Mwanayu akuchita nseru.
3