Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 3
Paphata pa Chichewa
Abathwa: Mawuwa amanenedwa monyoza anthu omwe
ndi aafupi. Dzinali lanayamba chifukwa cha mtundu wina
wa anthu akale omwe ankakhala afupiafupi. Anthuwo
ankatchedwa abathwa.
Chitsanzo: Sindimafuna kuti ana anga adzakwatiwe ndi
abathwa.
Achabechabe: Opanda ntchito.
Chitsanzo: Anthu amene aja ndi achabechabe.
Achinansi: Anthu owadziwa, achibale.
Chitsanzo: Uziyankhula bwino ndi alendo ungadzanyoze
achinansi.
Achitaiko (otaika): Anthu osokonekera.
Chitsanzo: Muzilalikira anthu achitaiko.
Adaminirako: Adaipitsako, anachita zoipa n’kuthawa.
Chitsanzo: Amakana kupita kumudzi chifukwa
adaminirako.
Adamulenga: Adasiya kuyenda naye.
Chitsanzo: Anthu amenewa ankagwirizana poyamba,
koma pano adalengana.
Adanka: Adapita.
Chitsanzo: Akuluakulu andanka kumanda ndi nzeru zawo
zomwe.
Adapinama: Adasintha khalidwe.
Chitsanzo: Poyamba mwamunayo ankakalipira mkazi
wakeyo, koma pano adapinama moti nayenso amabweza
zibakera.
2