Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 2

Paphata pa Chichewa Mawu Okuluwika ndi Zining’a za M’Chichewa Kalekale, dziko likali nsoka, akuluakulu ankakonda kusewera ndi mawu okuluwika komanso zining’a. Nthawi zina ankaponya mawu amenewa pofuna kupinda ana a makutu akuthwa kuti asatolepo kanthu pa zimene akukambirana. Makono, mikuluwiko imagwiritsidwa ntchito pofuna kutenderera chiyankhulo komanso pofuna kutchula mawu ena oumitsa pakamwa. Nkhani yopanda nsinjiro za chiyankhulo sikhala yothyakuka ndipo imakhala yopanda chikoka. Imangokhala ngati ndiwo zopanda mchere. M’bukuli muli zining’a, mawu okuluwika komanso mawu ena apatali a m’Chichewa. Mawu ena ndi omwe akugwiritsidwa ntchito kwambiri masiku ano. The Series Of Rodgers Bounty Books [RBB] Copyright © April 2016 by Bonwell “Kadyankena” Rodgers. All rights reserved. No part of this publication may be reproduced or transmitted in any form or by any means, electronical or mechanical, including photocopy, recording or any imformation storage and retrieval system, without permission in writing from the owner. Requests for permission should be mailed to: [email protected] Phone: 0881831435, 0881813953 1