Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 41
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Ukadzaona chipsolopsolo chikuyendayenda
pamudzi winawake, ndiye kuti chaona kansoti.
Chipumi bii: Mawu achipongwe onena za munthu yemwe
simukufuna mutamuona.
Chitsanzo: Kukadzakhala madyerero mudzamuona ali
chipumi bii, kubwera kudzadya nawo.
Chipumi: Mwana.
Chitsanzo: Amanenetsa kuti safuna kudzamwalira
asanasiye chipumi chawo padzikoli.
Chipupa:
(a) Khoma.
Chitsanzo: Chipupa cha nyumba chinawagwera.
(b) Munthu wosasunthika.
Chitsanzo: Amene uja ndi chipupa, simungamuthe.
Chipwirikiti: Chisokonezo.
Chitsanzo: Apolisi anaphulitsa utsi wokhetsa misozi ndipo
m’tauni monse munali chipwirikiti.
Chirombo: Munthu wamphamvu kwambiri kapena
munthu wankhanza mwinanso wouma kapena woipa
mtima.
Chitsanzo: Zimakhala zovuta kuti uzindikire kuti
munthuyu ndi chilombo mukakhala pachibwenzi.
Chisakasa: Chinthu chosamangidwa mwadongosolo
kwenikweni.
Chitsanzo: Amanga chisakasa chawo kumunda kuja.
Chisembwere: Chiwerewere.
Chitsanzo: Mayi opemphera aja anawagwira akuchita
zachisembwere.
40