Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 40
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Ataona kuti anzawo agula galimoto, nawonso
anakagula chiphapha chawo.
Chipheradzuwa: Mowa wolawa.
Chitsanzo: Akufuna muwapatse kaye chipheradzuwa.
Chiphuphamoyo: Kuvutika mumtima.
Chitsanzo: (1) Nditamva zoti akuvutika m’thupi,
ndinagona mwa chiphuphamoyo. (2) Ndikudwala moti
ndikungoyendera chiphuphamoyo.
Chiphuphu:
(a) Kupereka ndalama n’cholinga choti akukondere
kapena akuchitire chinachake chomwe samafunika
kukuchitira.
Chitsanzo: Anthu ambiri a m’boma amachita ziphuphu.
(b) Zilonda za pankhope.
Chitsanzo: Mwana akamakula amayamba ziphuphu.
Chipondam’thengo: Ndalama kapena chinachake
chomwe munthu amapereka kwa sing’anga asanapite
kukafuna mankhwala.
Chitsanzo: Mukamapita musaiwale kutenga kandalama
chifukwa ng’anga yake singakakuthandizeni popanda
kuipatsa chiponda mthengo.
Chipsinjo:
(a) Wosamva.
Chitsanzo: Mwana uyu ndi chipsinjo.
(b) Mavuto.
Chitsanzo: Anzanu aja ali pachipsinjo.
Chipsolopsolo: Mnyamata. Mawuna amatanthauzanso
tambala yemwe wangoyamba kumene kulira.
39