Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 42
Paphata pa Chichewa
Chisenjesenje: Kuchita kanthu usakudziwa chomwe
ukupanga.
Chitsanzo: Banja lawakanika. Anangokwatirira
chisenjesenje.
Chisi:
(a) Fungo la mbewa kapena nyama iliyonse
ikamaotchedwa.
Chitsanzo: (1) Anatipatsa masamba, koma pakhomopo
pamamveka chisi. (2) Koma ndiye atipha ndi chisi bwanji?
(b) Chilumba.
Chitsanzo: Chombocho chinasweka chisanafike pachisi.
Chisidze chodulira pansi: Mawu ankhunkhuniza kapena
okokomeza wonena za munthu wachinyengo, wokonda
akazi.
Chitsanzo: Pamene ankabwera pamudzi pano, palibe
ankadziwa kuti ndi chisidze chodulira pansi.
Chisimba: Nyumba.
Chitsanzo: Ndikumanga chisimba changa.
Chisimo: Chizolowezi chinachake.
Chitsanzo: Chisimo chanuchi chimandinyansa.
Chita chisira: Kulephera kukwatiwa, kupitirira pa
msinkhu wokwatiwa.
Chitsanzo: Osamakana amuna akakufunsirani,
mungachite chisira.
Chita gome: Chita manyazi.
Chitsanzo: Anthuwo atayamba kumuwowoza, anachita
gome.
Chita guni: Chita manyazi.
41