Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 329

Paphata pa Chichewa Pita panzeru: Kuposa wina pa nzeru. Chitsanzo: Anangochepa koma amakupitani panzeru. Pita poduka mphepo: Kupita popanda anthu, paokha. Chitsanzo: Tiyeni tikakumane poduka mphepo. Pokoma anatayira galu: Munthu wopanda pabwino, anthu akamuchitira zabwino iye amabweza zoipa. Chitsanzo: Mwana wanuyu alibe pabwino, pokoma anatayira galu. Pokonyola khosi (potola khosi): Kupotokola khosi la munthu. Chitsanzo: Zikuoneka kuti anamupha atamupokonyola khosi. Pokopoko: Phokoso la anthu omwe akukangana. Chitsanzo: Ndani angasangalale kuti pakhomo pake paz- ingozi pokopoko! Polaa: Kupolama. Chitsanzo: Tikaphe mpola, mbalame zili polaa! Polama: (a) Ima mowerama. Chitsanzo: Takaimani uko musalipolamire apa! (b) Ena amanena mawuwa potanthauza kuti akukumana ndi mavuto chifukwa cha Satana. Chitsanzo: Chaka chino Satana watipolamira. Ponda chitsononkho: Kulakwitsa chinachake. Chitsanzo: Munthu wina akaponda chitsonokho osamaseka, mawa ukhoza kudzakhala iwe. Ponda lupsa: Kukula, kuyamba kusamba kapena kutulutsa umuna. Chitsanzo: Wayamba kuvuta mmene waponda lupsamu. Ponda mabuleki: Ima kaye, siya kuchita zinthu zosa- longosoka. Chitsanzo: Nditaona kuti anthu ambiri akutenga 328