Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 328
Paphata pa Chichewa
Pintchapintcha: Kupintchama, kulephera kuyenda
bwinobwino.
Chitsanzo: Akuyenda pintchapintcha chifukwa wabinya.
Pinyolo: Kupereka chinthu chako kwa wina kuti
akupatse ndalama kapena chinachake.
Chitsanzo: Aponyoletsa njinga yawo.
Piringupiringu: Kumangoyendayenda kwa anthu
ochuluka.
Chitsanzo: Mmene ndimafika n’kuti anthu ali
piringupiringu.
Pisa khoswe mu ufa: Kusiyira mbala zinthu zomwe
akhoza kuziba.
Chitsanzo: Kumusiyira munthu ameneyu pakhomo pano
n’kupisa khoswe mu ufa.
Pisa m’maso: Kupita kukaona munthu kapena chinthu,
kuyendera munthu.
Chitsanzo: (1) Anabwera kuti akupiseni m’maso. (2)
Ndangoti ndidutseko kuti ndikupiseni m’maso.
Pisa m’matumba: Kukuthera ndalama, kukutengera
ndalama zonse.
Chitsanzo: Mukapanda kusamala akupisani m’matumba.
Pita kumanzere: Kukukanika, kusachita bwino zinazake.
Chitsanzo: Masewera a mpira anandipita kumanzere.
Pita kumwezi: Matenda a akazi omwe amadwala mwezi
ndi mwezi, kusamba.
Chitsanzo: Mkazi amayenera kuyala kampango pabedi
akapita kumwezi.
Pita padera (pita pachabe): Kubala mwana wakufa.
Chitsanzo: Zimandimvetsa chisoni mayi kudikirira miyezi
isanu ndi inayi n’kupita padera.
Pita pansi (yenda pansi): Namiza.
Chitsanzo: Apa ndiye mwandipita pansi (mwandiyenda
pansi), mugulitsa bwanji mbuzi osandiuza?
327