Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 330
Paphata pa Chichewa
kachilombo, ndinaganiza zoponda mabuleki.
Ponda mothudzula: Kupondereza.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani enafe amatiponda
mothudzula?
Ponda njati: Kutenga matenda kwa amuna kapena kwa
akazi.
Chitsanzo: (1) Ankangoti zungulizunguli ndi anyamata.
Pano anaponda njati ndipo akungokhala pakhomo. (2)
Masiku ano n’ngofunika kumayenda mosamala kuopera
kuponda njati.
Ponda pachilonda: Kuputa munthu, kuyambana.
Chitsanzo: (1) Simunganditero, mwandiponda pachilonda.
(2) Anthu aja anapondana pachilonda.
Ponda pakhosi: Kupha.
Chitsanzo: Amene wandibera ndalama zangazo
wandiponda pakhosi.
Ponda phazi limodzi kumanda: Tsala pang’ono kumwali-
ra.
Chitsanzo: Mukanamva zina ndithu, ndinaponda phazi
limodzi kumanda.
Pondaponda: Yendayenda.
Chitsanzo: (1) Ndatopa kukhala pakhomo pano. Ndikupita
kukapondaponda. (2) Muzipondaponda kuti ena akuoneni.
Pondera kuseri kwa phazi: Nyada.
Chitsanzo: Chifukwa choti kwawo ndi kochita bwino,
amangoyendera kuseri kwa phazi.
Ponya mwendo:
(a) Kuvina.
Chitsanzo: Nyimbo zotere zimakoma kuponya mwendo.
(b) Kuyenda mofulumira.
Chitsanzo: Kunjaku kwada, tiyeni tiponye mwendo.
329