Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 242
Paphata pa Chichewa
maso vinitsu.
Masomphenya: Kuoneratu zinthu zimene zidzachitike
m’tsogolo.
Chitsanzo: (1) Mulungu ankaonetsa anthu masomphenya.
(2) Tikufuna mtsogoleri wokhala ndi masomphenya.
Masuka ku chipsinjo: Kumasuka ku mavuto, kusiyana
ndi munthu wovuta.
Chitsanzo: Abwere adzamutenge mwana wawoyu kuti ndi-
masuke ku chipsinjochi.
Masweswe:
(a) Masewera.
Chitsanzo: Inetu sindingamachite masweswe ndi iwe,
ndine munthu wamkulu.
(b) Chiyambi cha dazi.
Chitsanzo: Umo mwadutsa masweswemo, ndi umboni wo-
ti akhoma malata m’mutumo posachedwapa.
Mata phula: Namiza.
Chitsanzo: Sindimadziwa kuti akundimata phula.
Matako piringidzane: Mawu onena monyoza za munthu
wopanda mnzeru yemwe simukufuna mutamuona.
Chitsanzo: Awotu akubwera apowo, ali matako
piringidzane!
Matakoakanapansi: Munthu woyendayenda.
Chitsanzo: Amene aja ndi a matakoakanapansi,
kamchacha weniweni.
Matambala: Ndalama zochepa.
Chitsanzo: Phindu limene ndapeza ndi timatambala.
Matangadza: Matabwa amene anthu amagwiritsira
ntchito pokhaulitsa munthu kuti asamayende kapena
kutakataka.
Chitsanzo: Ndinawapeza atawamanga m’matangadza.
241