Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 241

Paphata pa Chichewa Maso ali gegerere (maso ali yuu): Akundiyang’anitsitsa. Chitsanzo: (1) Mlanduwo uli mkati, bamboyo anatukwana ndipo maso onse anthu anangoti yuu, pa iye. (2) Umasuka bwanji maso a anthu ali gegerere. Maso ali ndi dumbo: Maso sakometsa zinthu. Mawu amenewa anabwera chifukwa cha bambo wina yemwe mkazi wake anamuphikira bowa wakudya ndipo iye anayamba kudandaula kuti ndiwo zake si zabwino. Koma atalawa anaona kuti ndiwozo ndi zokoma kwambiri ndipo anayankhula mawu amenewa. Chitsanzo: Ndimakaikira kuti zingakome, ndithu maso ali ndi dumbo. Maso apatali: Kusaonetsetsa kapena chinthu chosaoneka bwino. Chitsanzo: Sindimakudziwanitu, si nanga maso apatali. Maso kanthanga: Kumangoti wasankha ichi n’kuchisiya n’kumaonanso kuti china ndi chabwino kwambiri mpaka kutenga chosakhala bwino. Chitsanzo: “N’chifukwa chiyani mwagula malaya onyansa chonchi?” “Ndinachita maso kanthanga.” Maso mbuu: Kusowa chonena. Chitsanzo: Usati maso mbuu apa, mmesa ndinakutuman- so machesi! Maso mwazumwazu: Kuponya maso uku ndi uku. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani ukungoti maso mwazumwazu? Maso ndi maso: Kukumana ndi munthu weniweniyo. Chitsanzo: Ndikufuna nditakumana nawo maso ndi maso. Maso oboola ndi singano: Maso aang’ono kwambiri. Chitsanzo: Chinakusangalatsa n’chiyani pa amene uja? Maso oboola ndi singano aja? Maso vinitsu: Wandimana ndili pomwepo. Chitsanzo: Ndimaganiza kuti andigawira, koma anangoti 240