Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 243

Paphata pa Chichewa Matatalazi: Pamakhala mavuto ambiri, si zophweka. Chitsanzo: Kuti akubwereke ndalama pamakhala matatalazi. Matchiki: Mawu omwe achinyamata amanena akamanena za akazi. Chitsanzo: Matchiki a masiku ano sayankha ukawapatsa moni. Mate: Malovu. Chitsanzo: (1) Amayankhula ngati m’kamwa mwake mwadzadza mate. (2) Thawa apa ndikutsira mate. Matekenya: Matenda odyeka zala zakuphazi. Muzivala nsapato mungatenge matekenya. Matenda a boma: Matenda a Edzi. Chitsanzo: Ukapita kuchipatala mpamene umadziwa kuti anthu ambiri ali ndi matenda a boma. Matenda a kayakaya: Matenda oti mwina sachira. Chitsanzo: Ukaona azimayi akutuluka akumina m’nyum- ba momwe munali matenda a kayakaya, umangodziwira- tu kuti zavuta. Matenda amgonagona: Matenda okhalitsa. Chitsanzo: Pali anthu ambiri omwe akudwala matenda amgonagona m’dziko muno. Matenda akugwa: Matenda a khunyu. Chitsanzo: Mwanayu ali ndi matenda akugwa. Matenda osamva mankhwala: Matenda omwe sakuchita utamwa mankhwala. Chitsanzo: Matenda awo ndi osamva mankhwala. Matewe: Miyendo yopindika. Chitsanzo: Anthu amatewe amakhala amakani. Matsire: Kudzuka uli wofooka chifukwa cha mowa womwe unamwa dzulo. Chitsanzo: Aphikireni phala kuti achotse matsire. 242