Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 199
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Anzake amuthetsa makani.
Kuthetsa mankhalu: Kudabwitsa munthu, kukhaulitsa
munthu.
Chitsanzo: (1) Sindinaonepo munthu wokakamira chonchi
moti wandithetsa mankhalu. (2) Anamanga sukulu
mothetsa mankhalu.
Kuthetsa nzeru (kuthedwa nzeru): Kusowa chochita.
Chitsanzo: Mavutowa andithetsa nzeru.
Kuthiga: Kukhuta bwino, kukwanira bwino.
Chitsanzo: Amalemba Chichewa chothiga ndi nsinjiro za
chiyankhulo.
Kuthima:
(a) Kuledzera.
Chitsanzo: Ndinakumana nawo atathima.
(b) Kubaizika.
Chitsanzo: Pepani ndinathima, mumati chiyani?
(c) Kumwalira.
Chitsanzo: Munthu uja wathima.
Kuthimba pakhosi: Kuima pakhosi.
Chitsanzo: Mbatata yamuthimba pakhosi.
Kuthimbirira:
(a) Kuda kwambiri moti sizingayerenso.
Chitsanzo: Malaya anga athimbirira.
(b) Kusaoneka bwino chifukwa cha mavuto.
Chitsanzo: Mkazi wakwatiwa sabata yatha uja
wathimbirira kale.
Kuthimbwidzika: Kuyenda moyerekedwa.
Chitsanzo: Akumayenda mothimbwidzika ngati wamva zoti
pali amene akumufuna.
Kuthira māmadzi momwe: Kuuza munthu nkhani yomwe
akuidziwa kale.
Chitsanzo: Nkhaniyo inapheduka chifukwa atakumana
ndi mnzakeyo anamuuza zonse. Samadziwa kuti
198