Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 198

Paphata pa Chichewa Kuthandizana: Kugonana kwa anthu omwe sali pabanja kapena pachibwenzi n’cholinga choti angokhutiritsa chil- akolako chawo chakugonana. Chitsanzo: Achinyamata ambiri a ku koleji amathandi- zana. Kuthatha ndi imfa: Angotsala pang’ono kumwalira, akuphupha. Chitsanzo: Zimawawa kumaona wachibale akuthatha ndi imfa. Kuthatha: Kuphipha komwe kumachitika munthu akatsala pang’ono kumwalira. Chitsanzo: Zimakhala zochititsa mantha ukamaona mun- thu akuthatha. Kuthawa mtswatswa wako womwe: Kudabwa kapena kukana zomwe unaziyamba wekha. Chitsanzo: Ananena yekhatu, lero akuthawa mtswatswa wake womwe. Kuthawira pawindo: Kusiya sukulu. Chitsanzo: Ife sitinapite patali ndi sukulu, tinathawira pawindo. Kutheka: Kutopa. Chitsanzo: Koma ndiye wathekatu, pita ukagone! Kuthera m’manja: Kufera m’manja, kumenyedwa. Chitsanzo: Mwanayu adzathera m’manja. Kutheratu: (a) Kuonda kwambiri. Chitsanzo: Simungawadziwe pano, atheratu. (b) Kutoperatu. Chitsanzo: Ndayenda kwambiri moti ndatheratu. Kuthetsa anthu: Kuphetsa anthu. Chitsanzo: Mfumuyi ithetsa anthu ikapanda kuwateteza. Kuthetsa makani: Kumenya munthu kuti asiye kuchita mwano. 197