Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 200
Paphata pa Chichewa
akuthira m’madzi momwe.
Kuthothoka mapiko: Kutha mphamvu, kulephera ku-
chita zinazake.
Chitsanzo: (1) Munthu akayamba kutasa chonchi amafu-
nika kumuthothola mapiko. (2) Pano anafatsa chifukwa
anathothoka mapiko.
Kuthothoka nsidze: Kuchoka manyazi.
Chitsanzo: Nsungwanayu anathothoka nsidze.
Kuthowa: Kumenya munthu. Tanthauzo lake lenileni ndi
kufewetsa malo ovulala poikapo chinsanza chonyowa ndi
madzi otentha.
Chitsanzo: Amuthowa anzake.
Kuthyasika: Kumangotamanda munthu pongofuna ku-
musangalatsa.
Chitsanzo: Mayiwa ndi othyasika.
Kuthyolana bweya: Kuvitisana.
Chitsanzo: Chokani pano, musamathyolerane bweya
pakhomo panga pano!
Kuthyolera katsatsa: Kupereka ulemu.
Chitsanzo: Inu ndi akuluakulu, timakuthyolera katsatsa.
Kuthyolera m’thumba: Kuika chinthu m’thumba.
Chitsanzo: Atalandira ndalamazo anangozithyolera
m’thumba.
Kutiponya miyala: Kunyoza, kusiya kukulabadira.
Chitsanzo: Anzanu ajatu ayamba kutiponya miyala.
Kutisiya: Kumwalira.
Chitsanzo: Agogo anatisiya chaka chatha.
Kutokota:
(a) Kulongolola, kukalipira, kuyankhula kwambiri.
Chitsanzo: (1) Ndinawapeza akutokota. (2) Akazi awo aja
amatokota.
199