Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 181
Paphata pa Chichewa
Kupita kumanzere: Kusagwirizana nacho, kusakwanitsa
kuchita chinthu.
Chitsanzo: (1) Nyemba zinandipita kumanzere. (2)
Masewera a mpira anandipita kumanzere.
Kupita m’madzi (kulowa m’madzi): Kupita pachabe,
kungoonongeka.
Chitsanzo: Ndalama yanga yangolowa m’madzi.
Kupita mphepo:
(a) Kuzizira.
Chitsanzo: Chisiyeni chakudyachi chipite kaye mphepo.
(b) Kukhala kaye osadya.
Chitsanzo: Mwana iwe pakamwa pako padzipita mphepo!
Kupita pachabe:
(a) Kubereka mwana wakufa, kuchoka kwa mimba nthawi
yake isanakwane.
Chitsanzo: Mayiwa ali ndi vuto, akatu ndi kachitatu kupi-
ta pachabe.
(b) Kusagwira ntchito yake yoyenerera.
Chitsanzo: Khama langa langopita pachabe.
Kupita pansi: Kuchitira wina chiwembu, kupusitsa
munthu.
Chitsanzo: (1) Anthu a m’mudzi uno ayamba kundipita
pansi, ndiyenera kumakhala wosamala. (2) Atambwali
okhaokha sangapitane pansi.
Kupitana n’kupitana: Kuchitirana chipongwe,
kutukwanizana.
Chitsanzo: Anthu amenewa amapitana n’kupitana.
Kupitidwa mphepo ina: Kukaonako zina.
Chitsanzo: Ndipite kumudzi kuti ndikapitidwe mphepo
ina.
Kupola:
(a) Kuchira.
Chitsanzo: Bala langa silinapole.
180