Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 180
Paphata pa Chichewa
Kupindika nsana: Kukalamba.
Chitsanzo: Mtsikana wooneka bwino uja anapindika nsa-
na.
Kupindilana ndevu m’kamwa: Kukangana, kuvutitsana.
Chitsanzo: Akupindilana ndevu m’kamwa m’nyumbamu.
Kupindira ndevu m’kamwa: Kukhaulitsana. Nthawi zina
angatanthauzenso kupusitsa wina.
Chitsanzo: Akatswiri a nkhonyawo anapindirana ndevu
m’kamwa.
Kupindirana mashati: Kukangana.
Chitsanzo: Ndinawapeza atapindirana mashati.
Kupintchama: Kuyenda movutikira.
Chitsanzo: Ndakumana nawo akupintchama.
Kupinyoletsa: Kupereka katundu kwa wina utagwirizana
naye kuti ukapeza ndalamazo ukawombola katundu
wakoyo.
Chitsanzo: (1) Apinyoletsa njinga yawo ija. (2) Tsiku lina
adzapinyoletsa anawa kuti apeze ndalama ya mowa.
Kupirikitsa (kupitikitsa): Kuthamangitsa.
Chitsanzo: Awapirikitsamo m’nyumba muja.
Kupirikitsa: Kuthamangitsa.
Chitsanzo: Mukamavuta akupirikitsani pamudzi pano.
Kupiringa: Kupanga nthongo pogwiritsa ntchito manja.
Chitsanzo: Monse wayambira kupiringa mbamu muja,
ngati sukufuna kudya ingosiya!
Kupisira:
(a) Kulowetsa malaya m’kati mwa kabudula kapena
thirauza.
Chitsanzo: Pasukulu pano salola mwana wosapisira.
(b) Kuika manja m’matumba.
Chitsanzo: Akumadutsa apa atapisira m’matumba.
179