Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 182
Paphata pa Chichewa
(b) Kufunitsitsa utachita zinazake monga kubiba kapena
kudya. Nthawi zambiri zimenezi zimachitika moti sunga-
ziletse kuposa kuchita zimene thupi likufuna.
Chitanzo: (1) Manyi andipola. (2) Njala yandipola.
(c) Kuzizira.
Chitsanzo: (1) Mphala langa lapola. (2) Dikirani kaye kuti
tiyiyu apole.
Kupomboneza: Kusokoneza munthu.
Chitsanzo: Akungofuna kundipomboneza.
Kuponda: Kubwereka kapena kutenga chinthu cha wina
osamubwezeranso.
Chitsanzo: Amuponda ndalama zake zonse.
Kuponderezedwa: Kuchitiridwa zankhanza.
Chitsanzo: Anthu ambiri akuponderezedwa.
Kupotera: Kupitiratu, kutengedwa moti sizinga-
bwezedwenso.
Chitsanzo: Ndalama zanga zapotera.
Kupotera: Kutsakamira, kuuzidwa kuti
sadzakubwezeranso.
Chitsanzo: (1) Ndalama yako yapotera. (2) Ndalama zonse
zimene ndinawabwereka zija zinapotera.
Kupotoloka: Kubwerera.
Chitsanzo: Ndinabwera lija ndi kale, tsopano ndipotoloke.
Kupsa maere: Fulula thobwa kapena mowa.
Chitsanzo: Apsatu maere kumtundaku.
Kupsa mtima (kupsetsa mtima): kukwiya kwambiri,
kukwiyitsa wina kwambiri.
Chitsanzo: (1) Zimene achitazi zandipsetsa mtima. (2) An-
thu okondana aja anapsetsana mitima.
Kupsa ndevu: Kusauka.
Chitsanzo: Achimwene awo anapsa ndevu.
181