Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 174
Paphata pa Chichewa
Kupachika: Kuika wina pamavuto.
Chitsanzo: Pamenepatu ndiye mwandipachika! Zoona
mwawauzanso zimenezi!
Kupaka chipere: Namizira.
Chitsanzo: Ndikuona kuti anangomupaka chipere.
Kupaka: Kunena kuti walakwa koma asali iyeyo.
Chitsanzo: Mimbayi si yake, angomupaka.
Kupala pakamwa (m’kamwa): Kukuyamba.
Chitsanzo: (1) Akungofuna kundipala pakamwa. (2)
Anabwera n’cholinga choti adzangondipala m’kamwa.
Kupala pakamwa: Kubwera kudzakufunsa kapena kudza-
yankhula nawe kuti akutole zifukwa. Angatanthauzenso
kubwera kudzakuyamba.
Chitsanzo: Samabwera kudzacheza, anabwera kudzandi-
pala pakamwa.
Kupala:
(a) Kulephera.
Chitsanzo: Mdani wako akamapala umafunika ungomusi-
ya kuti amalizitse.
(b) Kuchotsa zimene zili pamwamba pa chinachake pog-
wiritsa ntchito chopalira.
Chitsanzo: Akupala mtengo.
(c) Kutenga moto n’kupita nawo kwina kuti ukaukoleze.
Chitsanzo: Ndimakapala moto.
(d) Kuputa kapena kuyamba munthu.
Chitsanzo: Amabwera kuti adzandipale mkamwa.
Kupalamula: Kulakwa, kuyambana ndi wina.
Chitsanzo: (1) Amene atabwere mochedwa wapalamula!
(2) Nkhope zina zimangooneka zopalamula kale chifukwa
cha mavuto.
Kupalapatika: Kungovutika pachabe.
Chitsanzo: Palibe chimene angachite ngakhale
titapalapatika bwanji?
173