Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 175
Paphata pa Chichewa
Kupalasa: Kuyenda kwambiri.
Chitsanzo: Sindingakwanitse kuyenda nawo limodzi chifu-
kwa amapalasa.
Kupambana: Kuwina, kukhoza.
Chitsanzo: Mwana wanu wapambana mayeso.
Kupana:
(a) Kukhala pachibwenzi, kufunsira.
Chitsanzo: Kodi Jemusi, wapana eti?
(b) Kuvulala utaphinyidwa kapena kupanikizidwa ndi
chinachake.
Chitsanzo: Chitseko chamupana.
Kupanda ungwiro: Kukhala munthu wochimwa,
kusakhala wangwiro, kukhala munthu wolephera kuchita
zinthu bwinobwino.
Chitsanzo: Anthu tonse ndi opanda ungwiro.
Kupapira: Kumwa madzi kapena mowa mosalekeza.
Chitsanzo: Wapapira mabotolo awiri a mowa.
Kupata: Kupeza.
Chitsanzo: Aulesi sangapate kanthu.
Kupatira: Haga, koloweka manja m’khosi mwa wina.
Chitsanzo: Muziwakupatira akazi anuwa.
Kupenekera: Kunena mosatsimikiza.
Chitsanzo: Ndikungopenekera kuti akhoza kukhala
anasamuka.
Kupepa kwa dzuwa: Kusiya kuwotcha kwambiri, cha-
kumadzulo.
Chitsanzo: Ndimakonda kuwongola miyendo dzuwa lika-
pepa.
Kupeputsa: Kunyoza, kuderera.
Chitsanzo: (1) Maso amapeputsa kolemera. (2) Sagwiri-
zana nanu chifukwa mumamupeputsa.
174