Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 173

Paphata pa Chichewa Kuonekera ng’amba: Kuonekera poyera. Chitsanzo: Achinyengo onse aonekera ng’amba. Kuonera pakhosi: Kutsala pang’ono kumwalira. Chitsanzo: Moyo tikungoonera pakhosipa. Kuonerana m’botolo: Kunyozana. Chitsanzo: Sindidziwa chifukwa chake amaonerana m’botolo. Kuonetsa mbwadza: Kukhaulitsa munthu. Chitsanzo: Anthu olusa amuonetsa mbwadza. Kuonetsa mfolo: Kuonetsa zoopsa, kuopseza munthu kuti amumenya. Mawuwa akamauza munthu wina ama- muuza kuti “udziwa mfolo.” Chitsanzo: Anzawo awaonetsa mfolo. Kuonetsa mpeni: Kupha. Chitsanzo: Mpofunika tambala ameneyu timuonetse mpeni. Kuonetsa nyenyezi: Kumenya moopsa moti n’kumaona ngati nyenyezi. Chitsanzo: Anzake a mowa anamuonetsa nyenyezi. Kuonjezera mchere (kuonjezera mchere): Kuonjezera zi- na. Chitsanzo: (1) Nkhani zolembedwa chonchi zimakhala zoti anaonjezeramo mchere. (2) Ndinadziwa kuti nkhaniyi aitsi- ra mchere. Kuotcha mtambo: Kupita dziko lina pandege. Chitsanzo: Chaka chino ndiotcha mtambo. 172