Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 9
Miyambi ya Patsokwe
Ali dere n’kulinga utayenda naye.
-Umboni weniweni umafunika kuchoka pa zimene waziona.
Ali ndi amayi anadala, amayenda monyada.
-Kukhala wamasiye n’kopweteka kwambiri. Makolo ndi ofunika
kuti mwana azisangalala komanso kuti akule bwino.
Ali ndi mwana agwiritse.
-Mawuwa amanenedwa pamene pabuka vuto lalikulu ndiye
wina akuchenjeza anzake kuti pakufunika kulimba nazo.
Mwambiwu unabwera chifukwa nthawi zambiri anthu akakhala
pamavuto, amayambirira kusamalira ana awo.
Ali patsogolo ali pambuyo pomwe.
-Munthu amene waima pamzere kutsogolo akhoza kukhala
kumbuyo ngati atauza anthuwo kuti atembenuke. Si bwino ku-
mathamangira zamtsogolo chifukwa chilichonse chili ndi nthawi
yake.
Ali patsogolo ndi amene ali pambuyo.
-Nthawi zina amene ali patsogolo amatha kukhala pambuyo
ngati anthuwo atauzidwa kuti atembunuke. Chimodzimodzi ndi
mwayi umene ena ali nawo, mawa zikhoza kutembenuka
n’kupezeka kuti ndi wathu.
Alibe pokomera, chili m’pokomera n’chirombo.
-Pali anthu ena omwe amati akathandizidwa amayambanso kun-
yoza amene awathandizawo. Anthu oterewa ndi oipa kuposa
chilombo chifukwa nthawi zina chilombo ukachichitira zabwino
chimayamika.
Aliona potuluka, polowa salipenya.
-Mawuwa amanenedwa poopseza munthu amene walakwira
mnzake kuti saliona dzuwa likamalowa chifukwa afa atalodzed-
wa. Mawuwa anabwera chifukwa cha zikhulupiriro za ku Africa
8