Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 10
Miyambi ya Patsokwe
kuno zoti anthu amalodza anzawo kapena kuwachesula kuti
akumane ndi zoopsa.
Aliyense adzadya thukuta lake.
-Munthu amafunika kulimbikira ntchito kuti apeze zimene aku-
funa.
Aliyense akondwa potsiriza.
-Munthu amasangalala akamaliza kugwira ntchito mwakhama
n’kulandira malipiro ake.
Amadziombera ng’oma yekha.
-Mawuwa amanena za munthu amene amakonda kuuza ena zo-
khudza zimene amachita komanso luso lake.
Amalume khalani pansi, ana akudziweni.
-Si bwino kumangokhalira kuyendayenda. Ndi bwino kumakha-
lako pakhomo nthawi zina.
Amapatsa mosiyana.
-Si bwino kusirira kapena kuchitira nsanje anzathu opeza bwino
kapena amene zikuwayendera.
Amene akufuna kuswa fupa amapita kuuzimba.
-Ukafuna chinthu umafunika kugwira ntchito. Kuti uswe fupa la
nyama umafunika kukasaka nyama kuthengo m’malo mongo-
longedza miyendo n’kumadikira kuti ikupeze pamene wakhala-
po.
Amene amagona kunsi kwa mwala, ndi amene amaona mwala
ukupuma.
-Ngati munthu ukufuna kumva zoona za zinthu ungachite
bwino kufunsa amene analipo pamene chinthucho chinkachi-
tika.
Amene umadya naye mbale imodzi ndi amene amakupereka.
-Mnzako amene umamukhulupirira ndi amene amakupereka
9