Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 11
Miyambi ya Patsokwe
kwa adani ako monga mmene zinachitikira ndi Yesu. Ana-
perekedwa ndi wophunzira wake.
Ana a ngoma opanda makutu.
-Mawuwa amanenedwa kwa ana osamvera. Amawayerekezera
ndi ana a ngoma omwe alibe makutu.
Anadya matako a galu.
-Si kawirikawiri kuona galu atakhala pansi ndi matako ake.
Nthawi zonse amangokhalira kuyendayenda. Ndiye munthu
akakhalanso kuti samakhala pansi, amangokhalira kuyendayen-
da amati, “anadya matako a galu.”
Anadya mtedza wa ching’onga.
-Mwambiwu umanena za munthu amene sachedwa kuiwala zin-
thu. Ching’onga chimati chikabisa kanthu chimaiwala msanga,
ndipo anthu amadzatola.
Anadya mtima wa Kalulu, nkona ali ndi mtima wokaluluka.
-Mwambiwu umanena za munthu amene ali ndi mtima wap-
achala, wosachedwa kupsa mtima.
Anadya mtima wa Sontho.
-Mwambiwu umanena za munthu amene amachita zinthu
mopupuluma kapena mofulumira kwambiri. Sontho ndi mbewa
imene imakonda kukhala m’makoko a chimanga chikakhala kuti
sichinakololedwe. Ndiyeno mbewayi imasonthoka ikamva pho-
koso la anthu okolola. N’chifukwa chake amaitchula kuti
Sontho. Choncho, chifukwa chakuti munthu wopupuluma
amachita zofanana ndi zimene mbewazi zimachita zikamathawa
m’makoko a chimanga, amangoti anadya mtima wa Sontho.
Anafa ndi nsanjikizo.
-Anthu akamanena za munthu amene wadzigwiritsa chifukwa
choti ananena zinthu zambirimbiri kapena ananena zinthu
10