Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 12
Miyambi ya Patsokwe
zomwe zamuika m’mavuto, amanena mwambiwu kuti, “Anafa
ndi nsanjikozo.” Mwambiwu umanenanso za munthu amene sa-
mamva kamodzi akalangizidwa.
Anafa wolongosola, aliko ndi kanthu umachita.
-Mwambiwu umanenedwa ngati mfumu yabwino kapena mun-
thu wina yemwe amachita bwino zinthu zinazake wamwalira.
Amaunena mfumu ina yosalongosoka ikakhala pampando
kapena wina akamagwira ntchito imene munthu anamwalira uja
ankagwira.
Anagula mbereko mwana asanabadwe.
-Mbereko ndi nsalu yoberekera kapena kufunditsa mwana
wakhanda. Mwambiwu umanena za munthu amene akuchita
zinthu mopupuluma nthawi yochitira zinthuzo isanakwane.
Anagulula nkhwangwa n’chambuyo.
-Mawuwa amanena za munthu wosabereka.
Anagwirizana malo okumana, koma anagona m’mitengo yo-
siyana.
-Mwambiwu umanenedwa ngati anthu ena omwe amayendera
limodzi asemphana chichewa n’kusiya kuyendera limodzi
kapena kusiya kugwirizana.
Anakhoma mutu wa Kalulu.
-Mutu wa Kalulu ndi wofewa moti kuukhoma suchedwa kuswe-
ka. Mwambiwu umatanthauza kupalamula mlandu.
Analawira m’mawa ndiye anapita.
-Anthu ena atanyanyalitsana, wina anangolawira kuchokapo.
Kukangana kumabalalitsa anthu.
Anamva ili m’mutu
-Mawuwa amanena za munthu amene amamva akakumana ndi
mavuto. Munthu wotero amakhala ngati wamva nkhwangwa ili
11