Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 13
Miyambi ya Patsokwe
m’mutu.
Anamwa tiyi adzamwanso, bola kusunga masupuni.
-Pamoyo wa munthu pamakhala mavuto, tikakhala pamavuto
tisamaganize kuti zinthu sizidzayendanso.
Anandimangira njoka m’masamba kuti andipweteke.
-Mwambiwu umanenedwa pamene anzako akuchitira zoipa
mwakabisira kuti ukumane ndi mavuto kapena akupweteke.
Ananditseka mawu kuti ndisayankhule.
-Mawu omwe amatanthauza kuti munthu ali ndi mawu, koma
kuti ayankhule, akumuletsa.
Anaotha chichiri cha tsimba.
-Tsimba ndi nyumba imene amasungirako mafumu olandira
udindo kapena anamwali. Chichiri ndi mtengo ndipo monga
mwa mwambo wa Achewa, mtengo umenewo kuuotcha ama-
khala malawulo. Mwambiwu umanenedwa munthu akapal-
amula pokwiyitsa anthu amene ankamuthandiza. Tsimba likho-
za kukhalanso nyumba yamasiye. Chifukwa cha zikhulupiriro,
anthu amaopa kuphikira kapena kuotha nkhuni zake. Ndiye
ngati munthu wina watenga nkhuni zake n’kuotha amamuona
kuti wapalamula. N’chifukwa chake munthu akapalamula anthu
amanena kuti, “Waotha chichiri cha tsimba.”
Anataya udzu womwetamweta.
-Mwambiwu umanena za munthu amene wataya mwawi chifu-
kwa chosakhazikika kapena kuyendayenda.
Anatsogoza mawu nyama isanafe.
-Mwambiwu umachenjeza anthu kuti azidikira kaye n’kuona
kuti zinthu zikhala bwanji m’malo mofulumira kuyankhula.
Anayamwira kubere.
-Nthawi zambiri munthu amatengera khalidwe kuchokera kwa
12