Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 8
Miyambi ya Patsokwe
kwa makolo ndipo makolowo ndi amene amavutika nalo.
Akuluakulu saika mtima pa imfa yako, nawenso umwalira
posachedwa.
-Osamafunira mnzako zoipa chifukwa nawenso zikhoza kuku-
chitikira.
Akunja n’kunkhokwe.
-Anthu ochokera kwina amakhala ngati nkhokwe chifukwa am-
abwera ndi zachilendo. Si chinthu chanzeru kumanyoza anthu
adera chifukwa nthawi zina ndi amene angatithandize kuthetsa
mavuto athu.
Akupempha, kali kutsaya.
-Mawuwa amanenedwa pamene munthu akupempha chikhulu-
lukiro kusonyeza kulapa koma n’kumapitirizabe kuchita zoipa.
Akupempha, lumo lili kumutu.
-Mawuwa amanenedwa wina akamalapa kapena kupepesa zin-
thu zitavuta kale.
Akuthawa mfuu yake yomwe.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu akukana ntchito kapena
cholakwa chomwe wachita. Mwachitsanzo mnyamata angakane
mtsikana amene wamuchimwitsa (popeza onse amakhala
achimwa mwina tinene kuti wachimwa naye).
Alendo akaipitsa m’nyumba, m’mawa agona kuti?
-Si bwino kuwononga zinthu pamalo amene tikukhala
tikumaganiza kuti sitikhalitsapo, chifukwa mawa tidzafunanso
kugona pomwepo.
Ali dere n’kulinga utayenda naye.
-Munthu umadziwa bwino makhalidwe a mnzako ngati utakha-
la naye limodzi kapena kuyenda naye.
7