Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 7
Miyambi ya Patsokwe
chifukwa akudziwa kale kuti zikamuvuta. Akamanena za mun-
thu wotereyu amati “akugwira chiputu kapena ziputu.”
Akukana kali kutsaya.
-Pali anthu ena amakana mlandu kapena zinthu zina m’maso
muli gwa ngakhale kuti pali umboni wonse wosonyeza kuti
achita ndi iwowo. Munthu akamakana zitafika pamenepa timati
akukana kali kutsaya.
Akula pusi wokhala patsekera.
-Pusi sangayende patsekera chifukwa ndi wamkulu kwambiri.
Chimodzimodzinso munthu wamkulu, sayenera kumachita
zachibwana kapena kumasewera ndi ana.
Akula vumbwe wotantha patsekera.
-Vumbwe sangayende patsekera chifukwa ndi wamkulu kwam-
biri. Chimodzimodzinso munthu wamkulu, sayenera kumachita
zachibwana kapena kumasewera ndi ana.
Akulu n’kudzala.
-Munthu wamkulu pamudzi kapena pantchito amakhala ngati
kudzala chifukwa nkhani zonse zimakathera kwa iye.
Akuluakulu amapempha ndi maso.
-Nthawi zambiri akuluakulu sachita kukuuza kuti uwathandize.
Amangokuyang’ana kuti wekha udziwe zochita. Mwambiwu
umanenedwa munthu wina wamkulu akachita zimenezi. Anthu
amati, “Tangowapatsani, akuluakulutu amapempha ndi maso!”
Akuluakulu ndi m’dambo mozimira moto.
-Moto wolusa umazima ukafika m’dambo chifukwa cha madzi
kapena chinyezi. Akuluakulunso amatha kuyanjanitsa anthu
akadana kapenanso kukhazikitsa mitima ya anthu pansi ngati
pali zina zovuta komanso kupereka malangizo abwino. Ko-
manso, nthawi zambiri ana akapalamula vuto lonse limafikira
6