Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 6
Miyambi ya Patsokwe
Akakhala mfulu ndi matenda, koma kapolo ndi ulesi.
-Chinthu chimodzi chomwecho chimatchulidwa mosiyasiyana
malinga ndi anthu ake. Munthu wolemera akhoza kutenga chin-
thu cha mwini n’kumati anangolakwitsa. Koma akakhala wo-
sauka amati waba.
Akam’meta n’kumva wapinama.
-Anamwali amaoneka ngati omvera komanso ofatsa ak-
amapatsidwa malangizo. Koma akangomaliza kuwapatsa
malangizowo, amakayambiranso makhalidwe awo oipa. Amai-
walilatu zimene analangizidwa zija. Mwambiwu umanena za
anthu amene samvera malangizo. Akalangizidwa amakhala nga-
ti amva, koma pakangopita nthawi amayamba kuchitanso zom-
we zija.
Akapsala sagulitsana nkhwangwa yoduka.
-Akamberembere sangapusitsane okhaokha. Mwachitsanzo, si
kawirikawiri akuba kuberana okhaokha.
Akapsala sapisana m’thumba.
-Nthawi zambiri, anthu a makhalidwe ofanana sangapusitsane.
Mwachitsanzo, si kawirikawiri akuba kuberana okhaokha.
Akayanjana aleke.
-Anthu amene amagwirizana nthawi zina amatha kuyambana
kapena kudana kumene. Zikatere chimene chimafunika ndi
kuyesetsa kuchita zinthu zoti agwirizanenso.
Akoma akadadza.
-Anthu amene poyamba amasonyeza makhalidwe abwino ke-
nako n’kuonetsa khalidwe lawo lenileni.
Akugwira ziputu.
-Mawuwa amanenedwa mophiphiritsa za munthu amene aku-
kana kuchoka pamalo kapena amene akukana kupita kumlandu
5