Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 5
Miyambi ya Patsokwe
Adatha mphika ndi “n’talawa.”
-Kukomedwa ndi chinthu kumapangitsa kuti uzolowere kenako
umatha kupalamula.
Adera amakoma podya nawo.
-Anthu adera amakonda munthu akakhala pabwino koma zik-
amuvuta kapena akasauka, amamuthawa. Achibale ake okha
ndi amene amamusamalabe.
Adye zabwino anadya zowawa.
-Mwambiwu umachenjeza munthu amene amafuna atapeza
zabwino zonse nthawi imodzi. Akapanda kusamala amatha ku-
kumana ndi mavuto. Choncho, zabwino zimabwera
pang’onopang’ono, munthu amangofunika kudikira kuti nthawi
yake ifike.
Adzidyera pamutu pa mfumu.
-Nthawi zina munthu amapeza mwayi chifukwa cha munthu
wina osati chifukwa cha khama lake lokha ayi.
Agona chimwini nsomba.
-Nsomba imakhala ngati yagona koma ikuona zonse zomwe zik-
uchitika. Mwambiwu umanenedwa munthu wina akamakhala
mosamala kapena akamagona makutu ali kunja poopa kuti ena
akhoza kumuchita chipongwe.
Akafuna kuchita, Kalulu azembera Galu.
-Pali anthu ena omwe amati akachita choipa amayamba
kunamizira osalakwa kapena omwe nkhaniyo sikuwakhudza.
Nthawi zambiri anthu ngati amenewa amaoneka ofatsa. Zimene
anthu oterewa amachita zikuyerekezedwa ndi zimene zingachi-
tike ngati Kalulu wachita chinachake choipa koma mlandu
n’kugwera Galu wosalakwa.
4