Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 4
Miyambi ya Patsokwe
Abwino sakhalitsa.
-Anthu abwino sakhala moyo nthawi yaitali.
Achimseka pachimera.
-Mwambiwu umanena za anthu amene amakonda munthu aka-
khala ndi chinachake choti awapatse monga zakudya, zakumwa
kapena zinthu zina zomwe akudziwa kuti akhoza kupindulapo.
Zinthuzo zikangomuthera amamutaya.
Achimseka pamaso, mumtima muli zina.
-Pali anthu ena omwe pamaso amaoneka ngati anzako, koma
kumbali amakudya miseche kapena kukukonzera zoipa. Ena
amakhala oti mumtima mwawo anakupha kalekale.
Achoke malizagudu, tiyanike inswa ziume.
-Mwambiwu umanenedwa ndi anthu omwe sakufuna kuti
anzawo akhalepo akamachita zinazake. Mwachitsanzo, akhoza
kukhala kuti akufuna aphike nsima koma sakufuna kuti
anzawowo adye nawo. Zikatero amadikira kaye enawo achoke
ndipo pouzana ndi amene amagwirizana nawo amati, “Dikirani
kaye, achoke malizagudu, tiyanike inswa ziume.” Mwambiwu
ukhoza kunenedwanso ngati wina akungofuna kuti achite zi-
nazake anthu ena akachoka.
Adadya Kalikongwe wa nzeru zayekha.
-Mwambiwu umanena za munthu amene samvera malangizo.
Nthawi zambiri munthu wotereyu amadzakumana ndi mavuto
kapenanso kufa kumene. Nkhani yake imanena za mbewa
yotchedwa Kalikongwe. Tsiku lina anzake ankaiuza kuti,
“Usakhale apa anthu angakuphe,” koma Kalikongwe
sanamvere. Anzakewo atachoka, kunabweradi anthu ndipo ata-
mupeza anamupha n’kukamudyera nsima.
3