Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 75
Miyambi ya Patsokwe
Zinthu zina zimachitika mwadzidzidzi chifukwa cha zinazake,
ndipo pambuyo pake zimadziwika.
Kalowa m’bwalo, sikatuluka.
-Zinthu zosangalatsa zimavuta kuzisiya.
Kalowa m’khutu kayala mphasa.
-Chomwe munthu wamva chimakhazikika.
Kalulu anamva mawu oyamba.
-Mawu oyamba ndi amene amakhala aphindu komanso ndi
amene anthu amagwira. Tizichenjera tikamanena zinthu chifu-
kwa anthu amagwira mawu anthu oyamba.
Kalulu anatuma njovu.
-Mwambiwu utanthauza pamene munthu wolemekezeka aku-
chita zinthu zina atatumidwa kapena m’malo mwa anthu ena
onyozeka.
Kamakuwa ndi kakumsampha, kam’diwa sikayankhula.
-Wina akagwidwa ndi ndalama yobedwa, sayankhula. N’zachi-
dziwikire kuti ndi amene anatenga ndipo amugwira basi.
Kamanenepetsa sikadziwika.
-Ndi bwino kumayesa njira zosiyanasiyana monga kulima ko-
manso kugwira ntchito. Osamangodalira chimodzi.
Kamanga zula.
-Ndi bwino kumathetsa zimene zikuyambitsa mavuto ako, vuto-
lo lisanakule.
Kamapikula nkhali ndi katsekera.
-Mwambiwu umanena za munthu amene amakonda kuchepetsa
zinthu, pomwe zotsatitira zake ndi zazikulu.
Kamata m’kati, ng’oma ya chimbulimbuli.
-Mawuwa amanena mokokomeza za munthu amene amaoneka
ngati wabwino pamaso koma mumtima mwake muli chiwembu.
74