Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 74
Miyambi ya Patsokwe
amavutika kwambiri. Palibe munthu amene angathe kuchita
zonse payekha, choncho ndi bwino kumadalirana.
Kalikonse kamakhala ndi chiyambi.
-Palibe chimene sichikhala ndi poyambira.
Kalikonse kouluka kamatera.
-Tingatchuke kapena kulemera bwanji, tsiku limadzafika loti ti-
madzasauka kapena kudzamwalira n’kusiyana nazo zonse.
Moyo umanyenga.
Kalindelinde adalinda chiswe.
-Mlesi amataya mwayi wogwira ngumbi pamene zituluka. Pope-
za wachedwa kudzuka, amapeza zatha ndipo amangopeza
chiswe.
Kalionera adaphika ntchentche kuyesa ana a Njuchi.
-Munthu ukamatengera makhalidwe oipa a anthu, amene uma-
kumana ndi mavuto ndi iweyo. Osamatengera zoipa zomwe ena
amachita.
Kalira-ulendo salira, ndi mtu uchepa.
-Munthu akamapita kwinakwake kukafuna zinthu monga
zovala kapena zakudya, amayenera kutenga zimene angapeze.
Akhoza kubwerera opanda kalikonse ngati atamaderera n’ku-
masiya zinthu.
Kalongoda sapsera madzi amodzi.
-Zinthu zina zimafunika khama kuti zitheke. Komanso kuti
munthu achite bwino amafunika kuthandizidwa kangapo.
Kalowa m’bwalo kali ndi nyimbo.
-Munthu akayamba kuchita zinazake ndiye kuti pali chimene
chikumulimbitsa mtima.
Kalowa m’bwalo kayanza malo.
-Zimakhala zovuta kuimitsa chinthu chimene chayamba kale.
73