Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 76
Miyambi ya Patsokwe
Kamba amanyerera amene wamtola.
-Pali anthu ena omwe umati ukawathandiza amabweza chipong-
we kapenanso kukubweretsera mavuto.
Kambalame kam’kamwa sikanona.
-Anthu ambiri sakonda kucheza ndi munthu wolongolola ndipo
nthawi zambiri munthu wotereyu amakhala wopanda khalidwe
ndipo anthu amamuthawa.
Kambalame kolawira kadakhuta nyongolotsi.
-Tikamayesetsa kuchita zinthu moyambirira, monga kulimba
munda, timapeza mphindu lalikulu. Koma ngati tayamba
mochedwa, timakumana ndi mavuto ambiri n’kupeza phindu
lochepa.
Kambaleme kochenjera sikachedwa kukoledwa paulimbo.
-Kuchenjeretsa komsamva nako malangizo kumaika munthu pa-
mavuto aakulu ngati mmene zimakhalalira ndi mbalame yomwe
imangoti zungulizunguli. Pamapeto pake imapezeka yakatera
paulimbo.
Kambuku sangasinthe manga ake.
-Zimakhala zovuta kuti munthu asiye zinthu zimene anazolow-
era.
Kambuzi kapambuyo kadalinda mkwapulo.
-Kuchita zinthu mochedwa kumapezetsa mavuto. Zimakhala
ngati mbuzi imene ili m’mbuyo, munthu akamafuna kukwapula
amakwapula imeneyoyo. Ndi bwino kumakhala patsogolo
pochita zinthu.
Kamodzikamodzi ndi mtolo.
-Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi zinthu zing’onozing’ono.
Mwambiwu umatiphunzitsanso kuti kuchita zinthu
mwachifatse n’kothandiza kusiyana n’kuchita zinthu
75