Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 29
Miyambi ya Patsokwe
kuchenjera pakakhala palibe mavuto, koma mavuto akagwa
amafuna kuti anthu ena amuthandize.
Chenjerechenjere sadzimeta, amakumeta ndi mnzako.
-Ngakhale munthu aoneke wochenjera motani, monga kuthawa
ntchito za gulu ngati pamaliro, tsiku lina zimadzamugwera
ndipo amadzafuna chithandizo cha ena.
Chenjerechenjere samapha nsomba, amapha nsomba n’kombe.
-Kuyankhula kwambiri pantchito sikusonyeza kuchenjera. Siku-
tanthauza kuti ntchito ikugwiridwa, koma kugwira ntchito n’ku-
mene kumayendetsa ndime.
Chenjerechenjere, anapsa ndi phala logona.
-Kusamva kapena kuchenjeretsa kumabweretsa mavuto aakulu.
Chete n’kunena (kukhala chete n’kunena).
-Pa mlandu munthu akafunsidwa koma osayankha, ndiye kuti
akuvomera kulakwa kwake.
Chetechete ndi upumbwa, akoma ndi suyosuyo.
-Tisamazengereze pogwira ntchito, koma kungogwiriratu pope-
za zamawa sizidziwika.
Chetechete sautsa nyama, autsa nyama n’kuwani.
-Ngati munthu wakasuma kukhoti, uyeneranso kulongosola tsa-
tanetsatane wa nkhani. Ngati sutero, mlanduwo ukhoza ku-
kuvuta.
Chetechete sautsa nyama, autsa nyama ndi suyo suyo.
-Kungokhala chete sikuthandiza ngati munthu ukufuna kukwa-
niritsa chinachake.
Chetechete sautsa nyama, koma suyosuyo.
-Kungokhala pamene mukuona zinthu zikulakwika sikuthandi-
za, koma kuyankhula kuti zinthu zikonzedwe.
28