Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 28

Miyambi ya Patsokwe Chapitamo wosenda luzi pamwala. -Mawuwa amanena za munthu wodziwa kwambiri mankhwala a zitsamba kuposa onse. Chati chubwi! chisati kapa! sichinaoloke. -Mawuwa amatanthauza kuti mawu oyamba ndi malonje chabe, nkhani yeniyeni sinayambe. Chati chubwi, sichinaoloke, koma chati kapakapa. -Mawuwa amatanthauza kuti mawu oyamba ndi malonje chabe, nkhani yeniyeni sinayambe. Chati deru chadabwitsa mlenje. -Kanthu sikachitika popanda chifukwa kapena choyambitsa chake. Ndiye kachizindikiro kangachepe bwanji, tizikhala nako tcheru. Chati deru chawopsa mlenje. -Munthu akasiya chizolowezi chake ndiye kuti chilipo chimene chamudabwitsa kapena chamuchititsa mantha. Chati khocho (tswa) sichinapite. -China chake chikakudabwitsa, khala tcheru. Chatuluka m’dzira n’chiyani? -Mwamuna akamakana kuti si amene anachimwitsa mkazi, an- thu amanena mawu amenewa pofuna kudziwa ngati mwana wobadwayo akufanana ndi mwamunayo. Pa mlandu uliwonse payenera kukhala umboni. Chauluka chidzatera. -Tingatchuke kapena kulemera bwanji, tsiku limadzafika loti ti- madzasauka kapena kudzamwalira n’kusiyana nazo zonse. Moyo umanyenga. Chenjerechenjere pa m’meto, pa maliro panalibe. -Mawuwa amanena za munthu amene amajijirika kapena 27