Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 27
Miyambi ya Patsokwe
Chaomba guta.
-Tsoka likagwera mlendo, anthu sadandaula kwenikweni. Koma
chisoni chimakula pamene wapamudzi pomwepo wakumana
ndi mavuto.
Chaona maso, mtima suiwala.
-Ndi bwino kumasamala ndi zimene timaona chifukwa zikhoza
kutigwetsera m’mavuto aakulu monga chigololo. Zimene mun-
thu waona amazikumbukira ngakhale patadutsa nthawi yaitali.
Chaona mchira gondwa ali m’mphako.
-Kusaonetsetsa kapena kusamvetsa zinthu kumapangitsa kuti
munthu azinena nkhani popanda umboni weniweni.
Chaona mnzako chapita, mawa chili pa iwe.
-Osamasangalala ena akamakumana ndi mavuto chifukwa na-
wenso akhoza kukupeza.
Chaona munda wakuthungo, mawa chidzaona munda wapaka-
ti.
-Munthu ukakhala pabwino umaona ngati sungadzavutike.
Nthawi zina munthu umatha kukumana ndi chinthu chimene
sumayembekezera kuti chingachitike.
Chaona mwana tola, ukulu n’kuona kako.
-Chaona mwana chitole chifukwa udzadya naye. Tisanyozere
chimene munthu amene ali pansi pathu wapeza, chifukwa
chikhoza kutithandiza.
Chaphulika chapsa, mkamwini konza nguwo.
-Chinthu chikachitika, monga imfa, pamafunika kulimba mtima
chifukwa chachitika chatha. Palibenso njira ina yochithetsera.
Chapita apa wachiona ndi munthu.
-Pa moyo wa munthu anthu ena ndi ofunika chifukwa amaku-
chenjeza.
26