Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 30
Miyambi ya Patsokwe
Chibale cha nkhondo, amawo akafa n’kumva ndiika nawo.
-Mawuwa amanena za munthu amene si m’bale wako weniweni,
koma chifukwa choti makolo anakhalira limodzi nthawi yaitali,
amakhala ngati m’bale wako weniweni.
Chibale n’chipsela.
-Chibale sichitha.
Chibale n’chipsera, sichitha.
-Sitingathe kuthetsa ubale, zivute zitani.
Chibale n’kuyenderana.
-Kuti chibale chilimbe pamafunika kuyenderana komanso
kuthandizana.
Chibale ndi fupa, sichiwola.
-Pangakhalitse abale osaonana, sikuti chibale chimatha.
Chibale ndi fupa.
-Chibale sichitha.
Chibale ndi litsiro, sichisansika.
-Chibale sichitha, abale amatha kuoneka ngati adana koma
amadzagwirizana.
Chibale pamowa.
-Anthu amene amakhala mabwenzi zikamayenda, koma pa-
mavuto amakuthawa.
Chibangiri chimapita ndi mwini dzanja.
-Sungakakamize munthu kuchita zimene sakufuna.
Chibwana chidatayitsa nguwo ya njuzi.
-Chifukwa cha chibwana, anthu amataya mwayi mwina wa ban-
ja kapena ntchito.
Chibwana n’chilonda, sichiona pokhala.
-Anthu achibwana amakhala paliponse ndipo zochita zawo
29