Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 237
Miyambi ya Patsokwe
Ukayenda siya phazi, ukasiya mlomo udzakutsata.
-Tikayenda tizisiya mbiri yabwino osati kuchoka titasokoneza.
Tisamanene mabodza.
Ukayendera nzengo usamati Asakhwi afumbula.
-Ukapita kukadula mitengo usaiwalenso chomwe wapitira
n’kuyamba kuyang’ana Asakhwi. Anthu amanena mwambiwu
ngati munthu amene watumidwa anayamba kuchita zina zosi-
yana ndi zimene anamuuza. Ukapita kwinakwake, usamayambe
kuchita zinthu zomwe sizinali cholinga chako.
Ukayipa nkhope, dziwa nyimbo.
-Ukazindikira kuti ndiwe wolephera pa chinachake, phunzira
kuchita chinthu china.
Ukaziputa limba.
-Osamayamba dala mavuto ngati ulibe podalira.
Ukaziputa, limba nazo.
-Ukamapalamula kapena kuyamba mavuto monga banja uma-
yenera kukhala utakonzeka kukumana ndi mavuto.
Uko kulire n’kumtsukwa.
-Mawuwa akutanthauza kuti kumene kukulira ndi kosongoka
kwa khasu. Pamene pali nkhani yeniyeni ndi pamene pama-
zunguza kwambiri.
Ukonde umayambira ku wakale.
-Poluka ukonde umangera ku wakale. Zinthu zatsopano zima-
yambira ku zakale.
Ukonzi unapha msemang’oma.
-Chisoni nthawi zina chimapezetsa mavuto kuchokera kwa an-
thu osayamika.
Uku kwawinda, tikudya mawa mande.
-Mawuwa amatanthauza kuti pali mapokoso kapena
236