Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 236
Miyambi ya Patsokwe
zimene munthu uja anakatenga ndi zimene zinam’phetsa.
Ukatambatamba uziyang’ana kum’mawa, kunja kungaku-
chere.
-Tikamachita zoipa monga kuba, chiwerewere tizizindikira kuti
akadzangotigwira tidzakumana ndi mavuto. Mwambiwu
umanena za kutamba chifukwa ena makolo akalelo
ankakhulupirira kuti afiti amatamba usiku.
Ukatchula Mkango, kwera m’mwamba.
-Ukamanena za munthu wina ndiye kuti ali pafupi. Mawuwa
amanenedwa ndi ena ngati njira yokupulumutsira kuti mun-
thuyo asakumve ukumunena. Anthu akamanena za munthu
wina, nthawi zambiri amakhala ali pafupi.
Ukatukwana ng’ona, kumadzi usapiteko.
-Ngati tapalamula timasowa mtendere mumtima podziwa kuti
chilango chikutidikira.
Ukayenda m’fumbi usadane n’kutuwa.
-Sitingathe kulekanitsa zinthu zoyendera limodzi monga fumbi
ndi kutuwa. Kumavomereza zinthu zina zikachitika.
Ukayenda m’tchire (m’thengo) wayendera zonse.
-Nthawi zina ukamayendera zina umathanso kuchita mwayi
wochitanso zina. Pamene munthu akupita kwinakwake
kukatenga chinthu, kumeneko amatha kukapezanso china
chomwe sanachiganizire ndipo ayeneranso kuchitenga.
Ukayenda ndi mwana wayenda wekha.
-Osamadalira kwambiri ana ukamachita zinthu.
Ukayenda panjira usamagulule mano, udzasowa chodyera
nyama.
-Tisanayambe kuchita chinthu tiziona kaye kuti tili ndi zonse zo-
funikira.
235