Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 238
Miyambi ya Patsokwe
chisokonezo ndiye anthu adya bwinobwino mawa zimenezi
zikatha. Ukamachita phwando ndi bwino kukonzekera chifu-
kwa anthu amawerengera kuti adzadya. Ena amachita kukhwe-
fula malamba awo kuti adzadye zambiri.
Ukufunsa za phula, njuchi ndi izi ukuziona.
-Mawuwa amanena za munthu amene akufunsa zinthu zoti aku-
zidziwa kale.
Ukukonda bwemba osakonda chulu!
-Usakonde bwemba koma chulu pamene pamera bwembayo.
Mawuwa amanena za mwamuna yemwe amakonda mkazi wake
yekha koma osati apongozi ake.
Ukulu si msinkhu ayi.
-Kutalika kapena kubadwa kale si nzeru koma kuchita kapena
kuyankhula zakupsa.
Ukundisokosera n’kulinga utamva.
-Mfundo za mawu timazipeza tikamvetsera kaye.
Ulemu n’kubadwa nawo.
-Tiyambiretu kuphunzitsa ana athu makhalidwe abwino adakali
aang’ono.
Ulemu n’kuthirana.
-Ukachitira wina ulemu nayenso amakupatsa ulemu.
Ulemu ndi mpira, umabwerera.
-Mawuwa amayerekezera ulemu ndi mpira womwe ukaulandira
umafunika kupatsira wina. Tizichitira ena ulemu, tikapanda ku-
wapatsa ulemu nawonso satipatsira mpira.
Ulemu wa Buluzi m’nyumba ya mfumu.
-Anthu ena amalandira ulemu chifukwa cha makolo komanso
anthu amene akukhala nawo, pomwe iwowo ndi onyozeka.
237