Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 17
Miyambi ya Patsokwe
Apawo ndi mchenga, madzi apita pansi.
-Munthu ukakhala mlendo sudziwa zomwe eni mudzi akupan-
gana, umangoona zikuchitika. Ali ngati mchenga omwe
sudziwika kuti pansi pake pali madzi. Choncho, ukakhala
pamudzi umayenera kusamala chifukwa nthawi zina amaoneka
ngati sagwirizana pomwe amagwirizana ndithu.
Apawo ndi mizu ya kachere, amakumana pansi.
-Munthu ukakhala mlendo sudziwa zomwe eni mudzi akupan-
gana, umangoona zikuchitika. Ali ngati mizu ya kachere yomwe
sudziwika kuti yakumana pansi. Choncho, ukakhala pamudzi
umayenera kusamala chifukwa nthawi zina amaoneka ngati sag-
wirizana pomwe amagwirizana ndithu.
Atadya anamwera.
-Chilichonse chimakhala ndi nthawi yake.
Atambala awiri salira m’khola limodzi.
-N’zovuta kuti anthu awiri azilamulira chinthu chimodzi.
Atambwali sametana, amaopa kuchekana.
-Nthawi zambiri anthu amene amachita zofanana zimakhala
zovuta kuti apusitsane. Atambwali sangapitane pansi.
Atambwali sametana, amawopa kuchekana.
-Ochenjera okhaokha sangapusitsane.
Aulesi sangapate kanthu.
-Palibe chinthu cholongosoka chimene munthu waulesi anga-
peze. Nthawi zambiri usiwa umamugwira munthu wotereyu
ngati kapolo.
Awonenji adapha mvuwu m’mono.
-Munthu aliyense ali ndi mwayi wake. Choncho, si bwino ku-
ganiza kuti anthu ena ooneka onyozeka sangapeze mwayi.
16