Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 16
Miyambi ya Patsokwe
Anyani amaonana zikang’a.
-Osamasekana wina akalakwitsa chifukwa nafenso nthawi zina
timalakwitsa ngati iyeyo. Mmalo mwake tizikhululukirana ndi
kulemekezana. Komanso si bwino kumanyoza kapena kuseka
ena pa zinthu zomwe nawenso umachita.
Anyani kuseweretsa magwafa.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamachita chibwana ndi zin-
thu zofunika kapena akamaseweretsa zinthu zofunika.
Anyani sasekana zikundu.
-Osamasekana wina akalakwitsa chifukwa nafenso nthawi zina
timalakwitsa ngati iyeyo. Mmalo mwake tizikhululukirana ndi
kulemekezana. Komanso si bwino kumanyoza kapena kuseka
ena pa zinthu zomwe nawenso umachita.
Aonenji adagwira kanthu mumdima.
-Anthu onyozeka amatha kuchita zinthu zomwe anthu odziwika
sangakwanitse monga kukhala olemera komanso kukhala ndi
banja labwino.
Aonenji anapha mvuu m’mono.
-Anthu ena amaoneka ngati onyozeka mwina chifukwa cha
kusauka ndipo ena sawathandiza poganizira kuti palibe chom-
we angadzawabwezere. Tsiku lina anthu otere amadzachita
chinthu chodabwitsa kapenanso kukhala ndi china chofunika.
Kuyeserera n’kofunika kusiyana ndi kungoyang’ana zinthu
poganiza kuti sizingatheke. Tisamapeputse nzeru za ena mpaka
titaona zotsatira zake.
Aonenji anapha njovu ndi mwala.

15