Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 15
Miyambi ya Patsokwe
aluso amachita. Amakonzera ena zinthu zabwino kwambiri
n’kumalephera kupanga zoti azigwiritsa ntchito iwowo.
Anthu muziwaopa, sali ndi miyendo inayi ngati Mkango.
-Tiyenera kulemekezana ngati anthu, chifukwa tsiku lina ti-
dzafuna anzathu kuti atithandize. Anthu sali ngati nyama
zakutchire zoti ungathe kuthawa mkwiyo wawo.
Anthu ndi mchenga sawundika.
-Anthu ena amakhala osadalirika. Ukapangana nawo zinthu
amachita zina.
Anthu ndi miyala sakukutika.
-Mwambiwu umasonyeza kuti nthawi zina, ngakhale anthu
uwachitire zabwino sathokoza. Nthawi zina amayambanso ku-
kunyoza kapena kukuchitira chipongwe ngati kuti ndi udindo
wako kuti uziwathandiza. Pomwe ena amakhala osadalirika.
Ukapangana nawo zinthu amachita zina.
Anthu ndi miyala sawundika.
-Anthu ena amakhala osadalirika. Ukapangana nawo zinthu
amachita zina.
Anthu oyanjana sagona manda amodzi.
-Mpofunika kumakondananso ndi anthu ena m’malo mon-
gokonda munthu m’modzi.
Anyang’wa a insa, aona ukonde waguluka.
-Anthu ochita zoipa monga ankhanza komanso akuba amaten-
gerapo mwayi akaona kuti mfumu kapena wolamulira ndi
wofatsa ndiponso woleza mtima, moti amayamba kuzunza
anzawo ndi kuchita zoipa zina zomwe sakanachita zikanakhala
kuti mfumu yake ndi yankhanza kapena yolamulira pomenya
matebulo.
14