Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 169
Miyambi ya Patsokwe
Mwala wogubuduzika sumera ndere.
-Kusakhazikika pamalo kapena pantchito kumachititsa kuti
tisapeze mwayi.
Mwala woyendayenda suyanga ndere.
-Kusakhazikika pamalo kapena pantchito kumachititsa kuti
tisapeze mwayi.
Mwalemera nyanga yanga simuidya.
-Munthu ukazolowera moyo wofewa mavuto suwaganizira.
Mwamuna koma kumuyang’ana kumimba.
-Mayi amayenera kudziwa kuti kuti mwamuna agwire ntchito
bwino amafunika kumupatsa chakudya.
Mwamuna mnzako mpachulu, umalinga utakwerapo.
-Osamaderera mnzako usanaone mphamvu zake, chifukwa
nthawi zina wonyozeka m’maso ndi amene amakutidzimula
kapena kukuposa pa chinachake.
Mwamuna mpamimba, nkhope siisintha.
-Mayi amayenera kudziwa kuti pakhomo kuti mwamuna agwire
ntchito bwino amafunika kumupatsa chakudya.
Mwamuna ndi kabudula, amathera moyenda.
-Mwamuna sakulira malo amodzi. Amafunika kuyendayenda
kuti akasake ndalama zothandizira mkazi komanso abale ake.
Mwamuna ndine ndekha adam’pachika ndi mkuzi.
-Osamadzikuza chifukwa ena akhoza kutichititsa manyazi ife
n’kunyowa.
Mwana akalilira fupa m’ninkhe.
-Nthawi zina ndi bwino kumalolera kuti ana achite zofuna
zawo. Ndi bwino kumaloleza maganizo kapena zimene anthu
ena akufuna kuti aphunzirepo kathu.
168