Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 168
Miyambi ya Patsokwe
Mvula yamvumbi kunyenga ana.
-Si bwino kutengeka ndi zinthu zomwe zimaoneka ngati si zoipa
kwenikweni. Zinthu ngati zimenezi zimachititsa kuti tidziimbe
mlandu kapena tikumane ndi mavuto ngati mmene mwana
amene wanyowa kapena wadzidetsa ndi matope a mvumbi
amachitira.
Mvumbi kwa ana, akulu nadya nthanga.
-Mawuwa amadzudzula khalidwe lodzikonda. Mwachitsanzo,
makolo kumadya kapena kumapeza zabwino ana ali pamvumbi,
kapena akuvutika.
Mvuu zikatha, amakankha bwato ndi kampango.
-Mavuto satherapo, akatha awa amabweranso ena.
Mwa limodzi anaonera khumi kutha.
-Nthawi zina mukagwira wakuba m’modzi amatha kuulula
anzake ambiri.
Mwachaje satafuna.
-Munthu sangatafune m’kamwa mopanda kanthu. Munthu wina
akamadandaula ndiye kuti pali vuto, tiyenera kumumvetsera.
Mwachaje satafuna.
-Ndi bwino kumakhutitsidwa ndi zimene uli nazo ngakhale zili
zochepa.
Mwakumbakumba mbewa mwalema, m’sakadandaule ndiwo.
-Munthu uyenera kuvomereza zotsatira za ntchito yako.
Mwachitsanzo, mbewa zikakukanika kukumba umasowa ndiwo
n’kuswera nayo njala.
Mwala umene amisili aukana umasanduka wapangodya.
-Nthawi zina zinthu zimene tikuziona kuti n’zosafunika zima-
khala zothandiza kwambiri.
167